spot_img
Monday, May 27, 2024
More
  HomeLatestA Billy Malata awona nyekhwe khoti litawatumiza ku ndende ya Maula poipitsa...

  A Billy Malata awona nyekhwe khoti litawatumiza ku ndende ya Maula poipitsa mbiri ya a ena pogwiritsa ntchito masamba a mchezo

  -

  Bwalo la milandu laling’ono ku Nathenje, latumiza mkulu woyang’anira nkhani za ndale m’chipani cha DPP, a Fredrick Billy Malata ku ndende ya Maula kwa masiku asanu ndi awiri (7).

  A Malata, adamangidwa loweruka pa mlandu woipitsa mbiri ya wochita malonda a Alfred Gangata pogwiritsa ntchito masamba a mchezo.

  Iwo adatengeredwa ku bwalo la milandu ku Nathenje dzulo ndipo bwalo lawatumiza ku Maula kwa amasiku 7 ponena kuti chigamulo pa pempho lawo la belo chidzapelekedwa Lachiwiri sabata ya mawa.

  Owayimilira a Malata a Gladwell Majekete atsimikiza za izi ndipo ati a Malata akasiyidwa ku Maula m’mawa wa lero atagona usiku wadzulo ku polisi ya Nathenje.

  Akulowa ku ndende ya Maula, a Malata adalankhura mwachidule ndi Times 360 Malawi ndipo anati: “Amalawi akufuna kwabwino andithandize. Ombudsman, a Chief Justice komanso Inspector General of police andithandize ndikuvutika. Ndagona ku Area 3 police masiku atatu, dzulo ndagona ku Nathenje lero akukandisiya ku Maula pa nkhani zosamveka. Panopa mu zovala zanga muli msikidzi zokhazokha, ndikuvutika.”

  Wolemba Cathy Maulidi

  Related articles

  LEAVE A REPLY

  Please enter your comment!
  Please enter your name here

  spot_img

  Latest posts